Eksodo 8:16 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Chauta adalamula Mose kuti, “Uza Aroni asamule ndodo yake ndipo amenye nthaka, motero fumbi lonse lidzasanduka nthata m'dziko lonse la Ejipito.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti akweze ndodo yake ndi kumenya fumbi la pa nthaka, ndipo fumbilo lidzasanduka nsabwe pa dziko lonse la Igupto.” |
Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.
Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu.
Koma pamene Farao anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
Ndipo anachita chomwecho; pakuti Aroni anasamula dzanja lake ndi ndodo yake, napanda fumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; fumbi lonse lapansi linasanduka nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.
Alembi anateronso ndi matsenga ao kuonetsa nsabwe, koma sanakhoze; ndipo panali nsabwe pa anthu, ndi pa zoweta.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tambasula dzanja lako ndi ndodo yako, pamtsinje, pangalande, ndi pamatamanda, nukweretse achule padziko la Ejipito.