Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 8:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti akweze ndodo yake ndi kumenya fumbi la pa nthaka, ndipo fumbilo lidzasanduka nsabwe pa dziko lonse la Igupto.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Pamenepo Chauta adalamula Mose kuti, “Uza Aroni asamule ndodo yake ndipo amenye nthaka, motero fumbi lonse lidzasanduka nthata m'dziko lonse la Ejipito.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 8:16
7 Mawu Ofanana  

Iye anayankhula, ndipo kunabwera ntchentche zochuluka ndi nsabwe mʼdziko lawo lonse.


Choncho ndikuti, ‘Mulole mwana wanga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana, Ine ndidzapha mwana wako wachisamba.’ ”


Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ”


Koma Farao ataona kuti zinthu zinayambanso kukhala bwino, anawumitsanso mtima wake ndipo sanamverenso mawu a Mose ndi Aaroni, monga momwe Yehova ananenera.


Iwo anachita momwemo, ndipo pamene Aaroni anakweza ndodo yake ndi kumenya fumbi, nsabwe zinafika pa munthu aliyense ndi pa ziweto. Fumbi lonse la mʼdziko la Igupto linasanduka nsabwe.


Koma amatsenga atayesa kupanga nsabwe mwa matsenga awo, analephera. Ndipo nsabwezo zinali pa munthu aliyense ndi pa ziweto zawo.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Loza ndodo yako ku mitsinje, ku ngalande ndi ku zithaphwi ndipo pakhale achule pa dziko lonse la Igupto.’ ”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa