Eksodo 7:21 - Buku Lopatulika Ndi nsomba za m'mtsinjemo zinafa; ndi mtsinjewo unanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'mtsinjemo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi nsomba za m'nyanjamo zinafa; ndi nyanjayo inanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'nyanjamo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nsomba zonse zamumtsinjemo zidafa, ndipo kununkha kwake kwa madziwo kunali kwakuti Aejipito sadathenso kuŵamwa. Ndipo munali magazi okhaokha m'dziko lonse la Ejipito. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nsomba za mu Nailo zinafa ndipo mtsinje unanunkha kwambiri kotero kuti Aigupto sanathe kumwa madzi ake. Magazi anali ponseponse mu Igupto. |
Ndi nsomba zili m'mtsinje zidzafa, ndi mtsinje idzanunkha; ndi Aejipito adzachita mtima useru ndi kumwa madzi a m'mtsinjemo.
Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m'mtsinjemo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake; ndipo madzi onse a m'mtsinjemo anasanduka mwazi.
Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.
Asodzinso adzalira, ndi onse oponya mbedza mu mtsinje adzaliralira, ndi onse oponya makoka m'madzi, adzalefuka.
ndipo lidafa limodzi la magawo atatu a zolengedwa zili m'nyanja, zokhala ndi moyo; ndipo limodzi la magawo atatu a zombo lidaonongeka.