Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao.
Eksodo 7:12 - Buku Lopatulika Pakuti yense anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti yense anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaponyanso pansi ndodo zao, ndipo zidasanduka njoka. Koma ndodo ya Aroni ija idameza ndodo zaozo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aliyense wa iwo anaponya ndodo yake pansi ndipo inasanduka njoka. Koma ndodo ya Aaroni inameza ndodo zawo. |
Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao.
Ndipo alembi sanathe kuima pamaso pa Mose chifukwa cha zilondazo; popeza panali zilonda pa alembi ndi pa Aejipito onse.
Koma sadzapitirirapo; pakuti kupusa kwao kudzaonekeratu kwa onse, monganso kupusa kwa iwo aja.
Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munaipambana; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;