Ndipo Mose anayankha nati, Koma taonani, sadzakhulupirira ine, kapena kumvera mau anga; pakuti adzanena, Yehova sanakuonekere iwe.
Eksodo 6:30 - Buku Lopatulika Koma Mose anati pamaso pa Yehova, Onani, ine ndili wa milomo yosadula ndipo Farao adzandimvera bwanji? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Mose anati pamaso pa Yehova, Onani, ine ndili wa milomo yosadula ndipo Farao adzandimvera bwanji? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Mose adauza Chauta kuti, “Inu mukudziŵa kuti paja ndine wosakhoza kulankhula, nanga Faraoyo adzandimvera bwanji?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Mose anati kwa Yehova, “Farao akandimvera bwanji, pakuti ine sinditha kuyankhula bwino?” |
Ndipo Mose anayankha nati, Koma taonani, sadzakhulupirira ine, kapena kumvera mau anga; pakuti adzanena, Yehova sanakuonekere iwe.
Ndipo Mose anati kwa Yehova, Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosowa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena chilankhulire Inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa m'kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera.
Koma Mose ananena pamaso pa Yehova, ndi kuti, Onani, ana a Israele sanandimvere ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula?
Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.