Udzu osawapatsa akapolo anu, ndipo amanena ndi ife, Umbani njerwa; ndipo, taonani, amapanda akapolo anu; koma kulakwa nkwa anthu anu.
Eksodo 5:17 - Buku Lopatulika Koma iye anati, Aulesi inu, aulesi: chifukwa chake mulikunena, Timuke, timphere nsembe Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iye anati, Aulesi inu, aulesi: chifukwa chake mulikunena, Timuke, timphere nsembe Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Farao adaŵayankha anthuwo kuti, “Ndinu alesi inu, alesi zedi, nchifukwa chake mukuti, ‘Tiyeni tipite tikapereke nsembe kwa Chauta.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Farao anati, “Ulesi, inu ndinu alesi! Nʼchifukwa chake mukumanena kuti, ‘Mutilole tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’ |
Udzu osawapatsa akapolo anu, ndipo amanena ndi ife, Umbani njerwa; ndipo, taonani, amapanda akapolo anu; koma kulakwa nkwa anthu anu.
Mukani tsopano, gwirani ntchito; pakuti sadzakupatsani udzu, koma muonetse chiwerengero chake cha njerwa.
Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musachepsapo, popeza achita ulesi; chifukwa chake alikufuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu.
Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.