Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 5:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musachepsapo, popeza achita ulesi; chifukwa chake alikufuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musachepsapo, popeza achita chilezi; chifukwa chake alikufuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma chiŵerengero cha njerwa chikhale chonchija, monga momwe ankaumbira kale. Musaŵachepetsere ndi pang'ono pomwe, ngaulesi ameneŵa. Nchifukwa chake akulira nkumati, ‘Tiyeni tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koma musawachepetsere chiwerengero cha njerwa chomwe munawalamulira kale kuti aziwumba. Iwowa ndi aulesi. Nʼchifukwa chake akulira kuti, ‘Tiloleni tipite tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 5:8
6 Mawu Ofanana  

Ndipo anawapereka m'manja a amitundu; ndipo odana nao anachita ufumu pa iwo.


Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.


Koma iye anati, Aulesi inu, aulesi: chifukwa chake mulikunena, Timuke, timphere nsembe Yehova.


Ndipo akapitao a ana a Israele anaona kuti kudawaipira, pamene ananena, Musamachepetsa njerwa zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake.


Musawapatsanso anthu udzu wakupanga nao njerwa monga kale; apite okha adzifunire udzu.


Ilimbike ntchito pa amunawo, kuti aigwiritsitse, asasamalire mau amabodza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa