Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;
Eksodo 5:13 - Buku Lopatulika Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani ntchito zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake, monga muja munali ndi udzu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani ntchito zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake, monga muja munali ndi udzu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akulu a Farao aja ogwiritsa ntchito, adafulumizitsa Aisraele naŵauza kuti, “Muziwumba chiŵerengero chonchija cha njerwa pa tsiku, monga munkachitira pamene ankakupatsani udzu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akapitawo a thangata aja anawafulumiza anthu aja nati, “Malizani kugwira ntchito yanu ya tsiku ndi tsiku monga mmene zinalili pamene munkapatsidwa udzu.” |
Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;
Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.
Mukani inu nokha, dzifunireni udzu komwe muupeza; pakuti palibe kanthu kadzachepa pa ntchito yanu.
Ndipo anapanda akapitao a ana a Israele, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsirize bwanji ntchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale?