Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 5:13 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Akapitawo a thangata aja anawafulumiza anthu aja nati, “Malizani kugwira ntchito yanu ya tsiku ndi tsiku monga mmene zinalili pamene munkapatsidwa udzu.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

13 Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani ntchito zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake, monga muja munali ndi udzu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani ntchito zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake, monga muja munali ndi udzu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Akulu a Farao aja ogwiritsa ntchito, adafulumizitsa Aisraele naŵauza kuti, “Muziwumba chiŵerengero chonchija cha njerwa pa tsiku, monga munkachitira pamene ankakupatsani udzu.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 5:13
7 Mawu Ofanana  

Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe zinalembedwera. Ankaperekanso nsembe za tsiku ndi tsiku monga mwa chiwerengero chake potsata mwambo wake wa tsiku ndi tsiku monga zinalembedwa.


Iye amakhala kutali ndi phokoso la mu mzinda; ndipo samva kufuwula kwa oyendetsa nyama zakatundu.


Kotero anayika akapitawo kuti aziwazunza ndi kuwagwiritsa ntchito yolemetsa mokakamiza. Iwo anamangira Farao mizinda ya Pitomu ndi Ramesesi kumene ankasungirako chakudya.


Mʼmalo mwake mupite mukadzimwetere udzu kulikonse kumene mungawupeze. Komabe ntchito yanu sichepetsedwa.’ ”


Kotero anthuwo anamwazikana mʼdziko lonse la Igupto kukamweta udzu.


Akapitawo a thangata a Farao ankawamenya oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja nawapanikiza kuti, “Chifukwa chiyani lero simunawumbe chiwerengero chovomerezeka cha njerwa monga chakale chija?”


Pa tsiku lomwelo Farao analamulira akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu kuti


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa