Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa chihema ndi guwa la nsembe, napachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza ntchitoyi.
Eksodo 40:8 - Buku Lopatulika Ndipo ukamange mpandawo pozungulira, ndi kupachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ukamange mpandawo pozungulira, ndi kupachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Upange bwalo kuzungulira chihemacho, ndi kukoloŵeka nsalu zochingira pa chipata chake cha bwalolo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Upange bwalo lozungulira chihemacho ndipo uyike katani ya pa chipata cha bwalolo. |
Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa chihema ndi guwa la nsembe, napachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza ntchitoyi.
Ukaikenso mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.
Pamenepo ukatenge mafuta odzoza, ndi kudzoza nao chihema, ndi zonse zili m'mwemo, ndi kumpatula, ndi zipangizo zake zonse; ndipo adzakhala wopatulika.
Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.
Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.