Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 40:9 - Buku Lopatulika

9 Pamenepo ukatenge mafuta odzoza, ndi kudzoza nao chihema, ndi zonse zili m'mwemo, ndi kumpatula, ndi zipangizo zake zonse; ndipo adzakhala wopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pamenepo ukatenge mafuta odzoza, ndi kudzoza nao Kachisi, ndi zonse zili m'mwemo, ndi kumpatula, ndi zipangizo zake zonse; ndipo adzakhala wopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Pambuyo pake utenge mafuta odzozera aja, udzoze Nyumba ya Mulungu ndi zonse za m'menemo. Uipereke kwa Mulungu Nyumbayo, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, kuti idzakhale yoyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Utenge mafuta wodzozera ndipo udzoze chihema ndi chilichonse chili mʼmenemo ndipo zidzakhala zoyeretsedwa.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 40:9
16 Mawu Ofanana  

Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa, chifukwa chake Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu ndi mafuta a chikondwerero koposa anzanu.


Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi chofukiza choona cha fungo lokoma, mwa machitidwe a wosakaniza.


guwa la nsembe la mkuwa, ndi sefa wake wamkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake;


Ndipo ukamange mpandawo pozungulira, ndi kupachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo.


Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;


Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;


Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali paphiri lopatulika la Mulungu, anayendayenda pakati pa miyala yamoto.


Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza chihema, ndi zonse zili m'mwemo, nazipatula.


Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kuutsa chihema, nachidzoza ndi kuchipatula, ndi zipangizo zake zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;


Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;


Pakuti Iye amene Mulungu anamtuma alankhula mau a Mulungu; pakuti sapatsa Mzimu ndi muyeso.


amenenso anatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu.


wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.


Ndiponso chihema ndi zotengera zonse za utumikiro anaziwaza momwemo ndi mwaziwo.


Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa