Eksodo 40:31 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ndi Aroni ndi ana ake aamuna anasamba manja ao ndi mapazi ao m'menemo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ndi Aroni ndi ana ake amuna anasamba manja ao ndi mapazi ao m'menemo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Mose, Aroni ndi ana ake adasamba m'manja natsuka mapazi ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo Mose, Aaroni ndi ana ake amasamba manja ndi mapazi awo. |
Ndipo anaika mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; nathiramo madzi osamba.
pakulowa iwo m'chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose.
Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai.
koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.
Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.