Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 40:25 - Buku Lopatulika

Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono pa choikaponyalecho adaikapo nyale, kuti zikhale pamaso pa Chauta, monga momwe Iye adalamulira Mose.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo anayikapo nyale zija pamaso pa Yehova, monga Yehova analamulira Mose.

Onani mutuwo



Eksodo 40:25
6 Mawu Ofanana  

Ndipo uzipanga nyali zake, zisanu ndi ziwiri; ndipo ayatse nyali zake, ziwale pandunji pake.


Ndipo anaika choikaponyali m'chihema chokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi.


Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikaponyalicho, ndi kuyatsa nyali zake.


Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali zisanu ndi ziwirizo ziwale pandunji pake pa choikaponyalicho.


Ndipo Aroni anachita chotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pake pa choikaponyali, monga Yehova adauza Mose.


Ndipo mu mpando wachifumu mudatuluka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za moto zoyaka kumpando wachifumu, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;