Nuziika gomelo kunja kwa nsalu yotchinga, ndi choikaponyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwera ya chihema; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto.
Eksodo 40:22 - Buku Lopatulika Ndipo anaika gomelo m'chihema chokomanako, pa mbali ya kumpoto ya Kachisi, kunja kwa nsalu yotchinga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaika gomelo m'chihema chokomanako, pa mbali ya kumpoto ya Kachisi, kunja kwa nsalu yotchinga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono m'chihema chamsonkhanomo adaikamo tebulo, chakumpoto kwa malo opatulika, kunja kwa nsalu yochinga ija, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anayika tebulo mu tenti ya msonkhano kumpoto kwa chihema, kunja kwa katani, |
Nuziika gomelo kunja kwa nsalu yotchinga, ndi choikaponyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwera ya chihema; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto.
Ndipo anaika choikaponyali m'chihema chokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi.
Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikaponyalicho, ndi kuyatsa nyali zake.
Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;