Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 40:18 - Buku Lopatulika

ndipo Mose anautsa chihema, nakhazika makamwa ake, naimika matabwa ake, namangapo mitanda yake, nautsa mizati ndi nsanamira zake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndipo Mose anautsa Kachisi, nakhazika makamwa ake, naimika matabwa ake, namangapo mitanda yake, nautsa mizati ndi nsanamira zake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Poutsa malowo, Mose adakhazika masinde ake pansi, ndipo adautsa mafulemu ake, nalumikiza mitanda yake, nautsanso nsanamira zake zija.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nthawi imene Mose anayimika chihema, anayika matsinde mʼmalo ake, kuyimitsa maferemu, kulowetsa mitanda ndi kuyika nsichi.

Onani mutuwo



Eksodo 40:18
15 Mawu Ofanana  

Pakuti sindinakhale m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinatulutsa ana a Israele ku Ejipito kufikira lero lomwe, koma ndinayenda m'chihema ndi m'nyumba wamba.


Ndipo kunali, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa chihema,


Ndipo anayalika hema pamwamba pa Kachisi, naika chophimba cha chihema pamwamba pake; monga Yehova adamuuza Mose.


Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse Kachisi wa chihema chokomanako.


Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala m'menemo, adzakhululukidwa mphulupulu zao.


Ndidzamanga Kachisi wanga pakati pa inu, ndipo moyo wanga sudzanyansidwa nanu.


Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,


kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.


amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;