Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 4:8 - Buku Lopatulika

Ndipo kudzatero, ngati sakhulupirira iwe, ndi kusamvera mau a chizindikiro choyamba, adzakhulupirira mau a chizindikiro chotsirizachi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo kudzatero, ngati sakhulupirira iwe, ndi kusamvera mau a chizindikiro choyamba, adzakhulupirira mau a chizindikiro chotsirizachi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pamenepo Chauta adati, “Akakapanda kukukhulupirira, osasamala chizindikiro choyambacho, akakhulupirira ndithu chifukwa cha chizindikiro chachiŵiricho.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsono Yehova anati “Akakapanda kukukhulupirira, osalabadira chozizwitsa choyambacho, akakhulupirira ndithu chifukwa cha chozizwitsa chachiwiricho.

Onani mutuwo



Eksodo 4:8
10 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali atawerenga kalatayo mfumu ya Israele, anang'amba zovala zake, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumchiritsa munthu khate lake? Pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna chifukwa pa ine.


Pakuti apweteka, namanganso mabala; alasa, ndi manja ake omwe apoletsa.


Ndipo Mose anauza Aroni mau onse a Yehova amene adamtuma nao, ndi zizindikiro zonse zimene adamlamulira.


Ndipo ananena iye, Bwerezanso dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo anabwerezanso dzanja lake pachifuwa pake; nalitulutsa pachifuwa pake, taonani, linasandukanso lomwe lakale.


Ndipo kudzatero, akapanda kukhulupirira zingakhale zizindikiro izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kumtsinje ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku mtsinjewo adzasanduka mwazi pamtunda.


Pakuti pali langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono.


Koma angakhale adachita zizindikiro zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirire Iye;


Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.


Ndipo anati kwa Iye, Ngati mundikomera mtima mundionetse chizindikiro tsopano chakuti ndi Inu wakunena nane.