Eksodo 4:29 - Buku Lopatulika Pamenepo Mose ndi Aroni anamuka nasonkhanitsa akulu onse a ana a Israele; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Mose ndi Aroni anamuka nasonkhanitsa akulu onse a ana a Israele; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Mose ndi Aroni adapita, nakasonkhanitsa atsogoleri onse a Aisraele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose ndi Aaroni anapita kukasonkhanitsa pamodzi akuluakulu onse a Aisraeli. |
Ndipo Mose anadza, naitana akulu a anthu, nawaikira pamaso pao mau awa onse amene Yehova adamuuza.
Ndipo Iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali;
Koma sanatulutse dzanja lake pa akulu a ena a Israele; ndipo anapenya Mulungu, nadya, namwa.
Muka, nukasonkhanitse akulu a Israele, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndakuzondani ndithu, ndi kuona chomwe akuchitirani mu Ejipito;