Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.
Eksodo 39:24 - Buku Lopatulika Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa mpendero wake wapansi, adalumikizapo zithunzi za makangaza zopangidwa ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, analumikiza mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yofewa yosalala ndi yopetedwa bwino yomwe inazungulira mkanjo. |
Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.
Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolide pozungulira;
ndi pakati pake polowa mutu, ngati polowa pa malaya ochingirizira, ndipo anabinyira pozungulira polowa pake, pangang'ambike.
Ndipo anapanga miliu ya golide woona, napakiza miliu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,