Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 28:33 - Buku Lopatulika

33 Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolide pozungulira;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolide pozungulira;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Pa mpendero wapansi wa mkanjowo, upange zinthu zonga makangaza. Zikhale za thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, kuzungulira mkanjo wonsewo. Pakati pa makangazawo pakhale timabelu tagolide.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, upange mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira zokhala ndi maberu agolide pakati pake.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:33
7 Mawu Ofanana  

M'mwemo anapanga nsanamira, ndipo panali mizere iwiri yozungulira ukonde umodzi, kukuta ndi makangaza mituyi inali pamwambapo, nachita momwemo ndi mutu winawo.


Msinkhu wake wa nsanamira imodzi ndiwo mikono khumi mphambu isanu ndi itatu, ndi pamwamba pake mutu wamkuwa; ndi msinkhu wake wa mutuwo ndiwo mikono itatu, ndi ukonde, ndi makangaza pamutu pouzinga, zonse zamkuwa; ndi nsanamira inzake inali nazo zomwezo pamodzi ndi ukonde.


Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.


Ndipo polowa mutu pakhale pakati pake; pakhale mkawo pozungulira polowa pake, wa ntchito yoomba, ngati polowa pa malaya otchinjiriza, pangang'ambike.


mliu wa golide ndi khangaza, mliu wagolide ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira.


Tsiku lomwelo padzaoneka pa miliu ya akavalo Opatulikira Yehova; ndi mbiya za m'nyumba ya Yehova zidzanga mbale za kuguwa la nsembe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa