Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 28:34 - Buku Lopatulika

34 mliu wa golide ndi khangaza, mliu wagolide ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 mliu wa golide ndi khangaza, mliu wagolide ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Choncho pakhale khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, kuzungulira mpendero wonse wam'munsiwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Choncho pazikhala mphonje imodzi kenaka belu limodzi, kuzungulira mpendero wa mkanjo wonse.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:34
15 Mawu Ofanana  

Odala anthu odziwa liu la lipenga; ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.


Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolide pozungulira;


Ndipo Aroni auvale kuti atumikire nao; ndipo limveke liu lake pakulowa iye m'malo opatulika pamaso pa Yehova, ndi pakutuluka iye, kuti asafe.


Ndipo anaomba mwinjiro wa efodi, ntchito yoomba ya lamadzi lokha;


Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose.


Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aamuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake, zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga.


Mphukira zako ndi munda wamakangaza, ndi zipatso zofunika, bonongwe ndi narido.


Milomo yako ikunga mbota yofiira, m'kamwa mwako ndi kukoma: Palitsipa pako pakunga phande la khangaza paseri pa chophimba chako.


Ndinatsikira kumunda wa mtedza, kukapenya msipu wa m'chigwa, kukapenya ngati pamipesa paphuka, ngati pamakangaza patuwa maluwa.


Palitsipa pako pakunga phande la khangaza paseri pa chophimba chako.


Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m'nyumba ya amai, kuti andilange mwambo; ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa, ndi madzi a makangaza anga.


Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.


kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa