Eksodo 39:10 - Buku Lopatulika Ndipo anaika pomwepo mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaika pomwepo mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adaikapo mizere inai ya miyala yokongola. Pa mzere woyamba adaika miyala ya rubi, topazi ndi garaneti. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anayikapo mizere inayi ya miyala yokongola kwambiri. Mzere woyamba anayika miyala ya rubi, topazi ndi berili; |
Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga maina ao; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.
Chinakhala chaphwamphwa; anachiomba chapachifuwa chopindika; utali wake dzanja limodzi, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi, chinakhala chopindika.