Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 28:21 - Buku Lopatulika

21 Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga maina ao; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga maina ao; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Miyala imeneyi ikhalepo khumi ndi iŵiri, potsata maina a mafuko a Aisraele. Miyalayo izokotedwe ngati zidindo, uliwonse ukhale ndi dzina la fuko limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Miyalayo ikhalepo khumi ndi iwiri, uliwonse kuyimira dzina limodzi la ana a Israeli. Mwala uliwonse uzokotedwe ngati chidindo dzina limodzi la mafuko khumi ndi awiri a Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:21
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya anatenga miyala khumi ndi iwiri, monga mwa ziwerengo cha mafuko ana a Yakobo, amene mau a Yehova adamfikira, kuti, Dzina lako ndi Israele.


Akadawazokota pathanthwe chikhalire, ndi chozokotera chachitsulo ndi kuthira ntovu!


Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde paphiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele.


Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.


ndi mzere wachinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golide m'zoikamo zao.


Upangenso maunyolo pa chapachifuwa ngati zingwe, ntchito yopota, ya golide woona.


Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ake; pakuti adzakhala ngati miyala ya m'korona yakunyezimira padziko lake.


ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.


Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'chibalaliko: ndikupatsani moni.


nukhala nalo linga lalikulu ndi lalitali, nukhala nazo zipata khumi ndi ziwiri, ndi pazipata angelo khumi ndi awiri, ndi maina olembedwapo, ndiwo maina a mafuko khumi ndi awiri a ana a Israele;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa