Eksodo 38:7 - Buku Lopatulika Ndipo anapisa mphikozo mu mphetezo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapisa mphikozo m'zimphetemo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono guwalo pomalinyamula, mphikozo ankazilonga m'mphete zija, pa mbali zonse ziŵiri za guwa. Guwalo adalipanga ndi matabwa, ndipo adalijoba m'kati mwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo analowetsa nsichizo mʼmphetemo mbali zonse ziwiri za guwalo kuti azinyamulira. Guwalo linali lamatabwa ndi logoba mʼkati mwake. |
Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako.
Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israele;
koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Agriki, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.
Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu mwa inu, koma Yesu Khristu, ndi Iye wopachikidwa.