Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:15 - Buku Lopatulika

15 Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israele;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israele;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Koma Ambuye adamuuza kuti, “Pita, pakuti iyeyu ndi mtumiki wanga amene ndidamsankha kuti akalalikire dzina langa anthu a mitundu ina, mafumu, ndiponso Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Koma Ambuye anati kwa Hananiya, “Pita! Munthu uyu ndi chida changa chosankhika chonyamulira dzina langa pamaso pa anthu a mitundu ina ndi mafumu awo ndiponso kwa anthu a Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:15
38 Mawu Ofanana  

Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.


Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.


ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.


Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.


Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.


Ndipo atawalonjera iwo, anawafotokozera chimodzichimodzi zimene Mulungu anachita kwa amitundu mwa utumiki wake.


Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe chifuniro chake, nuone Wolungamayo, numve mau otuluka m'kamwa mwake.


Ndipo anati kwa ine, Pita; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.


Ndipo Agripa anati kwa Fesito, Ndifuna nanenso ndimve munthuyo. Anati, Mawa mudzamva iye.


Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Kwaloleka udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, anatambasula dzanja nadzikanira:


Ndipo Agripa anati kwa Fesito, Tikadakhoza kumasula munthuyu, akadapanda kunena, Ndikatulukire kwa Kaisara.


nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.


Ndipo kunali, atapita masiku atatu, anaitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, ananena nao, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindinachite kanthu kakuipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, anandipereka wam'nsinga kuchokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma;


Potero, dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwa amitundu; iwonso adzamva.


Paulo, kapolo wa Yesu Khristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,


amene ife tinalandira naye chisomo ndi utumwi, kuti amvere chikhulupiriro anthu a mitundu yonse chifukwa cha dzina lake;


Koma ndilankhula ndi inu anthu amitundu. Popeza ine ndili mtumwi wa anthu amitundu, ndilemekeza utumiki wanga;


Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.


Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.


Paulo, mtumwi (wosachokera kwa anthu, kapena mwa munthu, koma mwa Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate, amene anamuukitsa Iye kwa akufa),


Chifukwa cha ichi ine Paulo, ndine wandende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu amitundu,


umene anandiika ine mlaliki wake ndi mtumwi (ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi wa amitundu m'chikhulupiriro ndi choonadi.


umene ndaikikapo mlaliki, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wake.


Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali.


Iwo adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawagonjetsa, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa