Eksodo 37:7 - Buku Lopatulika Anapanganso akerubi awiri agolide; anachita kuwasula mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anapanganso akerubi awiri agolide; anachita kuwasula mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa nsonga zake ziŵiri za chivundikirocho, adazokotapo akerubi aŵiri a golide wosula ndi nyundo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anapanga Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo ndi kuwayika mbali ziwiri za chivundikirocho. |
Mbusa wa Israele, tcherani khutu; inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; inu wokhala pa akerubi, walitsani.
Ndipo anapanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu.
kerubi mmodzi pa mbali yake imodzi, ndi kerubi wina pa mbali yake ina; anapanga akerubi ochokera m'chotetezerapo, pa mathungo ake awiri.
Ndipo Yehova analankhula ndi munthu wovala bafuta, nati, Lowa pakati pa njingazi pansi pa kerubi, nudzaze manja ako makala a moto ochokera pakati pa akerubi, nuwamwaze pamwamba pa mzinda. Nalowa, ndili chipenyere ine.