Ndipo mphikozo zinatalika kuti nsonga za mphiko zidaoneka ku malo opatulika chakuno cha chipinda chamkati; koma sizinaoneke kubwalo; ndipo zikhala pomwepo mpaka lero lino.
Eksodo 37:5 - Buku Lopatulika Ndipo anapisa mphiko m'mphetezo pa mbali zake za likasalo, kuti anyamulire nazo likasa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapisa mphiko m'mphetezo pa mbali zake za likasalo, kuti anyamulire nazo likasa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo mphikozo adazipisa m'mphete zija pa mbali zonse ziŵiri za bokosilo, kuti azinyamulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo analowetsa nsichizo mʼmphete zija za mbali zonse ziwiri za bokosilo kuti azinyamulira. |
Ndipo mphikozo zinatalika kuti nsonga za mphiko zidaoneka ku malo opatulika chakuno cha chipinda chamkati; koma sizinaoneke kubwalo; ndipo zikhala pomwepo mpaka lero lino.
Ndipo anapanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu.
koma iwe, uike Alevi asunge chihema cha mboni, ndi zipangizo zake zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula chihema, ndi zipangizo zake zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa chihema.
Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.