Ndipo ana a Alevi anasenza likasa la Mulungu pa mapewa ao, mphiko zili m'mwemo, monga Mose anawauza, monga mwa mau a Yehova.
Eksodo 37:3 - Buku Lopatulika Ndipo analiyengera mphete zinai zagolide pa miyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake imodzi, ndi mphete ziwiri pa mbali yake ina. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo analiyengera mphete zinai zagolide pa miyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake imodzi, ndi mphete ziwiri pa mbali yake ina. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adapanga mphete zinai zagolide zonyamulira, nazimangirira ku ngodya zinai za bokosilo, uku ziŵiri uku ziŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anapanga mphete zinayi zagolide ndi kuzimangirira ku miyendo yake inayi ija, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri. |
Ndipo ana a Alevi anasenza likasa la Mulungu pa mapewa ao, mphiko zili m'mwemo, monga Mose anawauza, monga mwa mau a Yehova.
Pakuti akerubi anafunyulula mapiko ao pamalo a likasa, ndi akerubi anaphimba likasa ndi mphiko zake pamwamba pake.
ndipo analikuta ndi golide woona m'kati ndi kunja, nalipangira mkombero wa golide pozungulira pake.
Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.