Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 37:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Iye anapanga mphete zinayi zagolide ndi kuzimangirira ku miyendo yake inayi ija, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo analiyengera mphete zinai zagolide pa miyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake imodzi, ndi mphete ziwiri pa mbali yake ina.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo analiyengera mphete zinai zagolide pa miyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake imodzi, ndi mphete ziwiri pa mbali yake ina.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Adapanga mphete zinai zagolide zonyamulira, nazimangirira ku ngodya zinai za bokosilo, uku ziŵiri uku ziŵiri.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 37:3
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Alevi ananyamula Bokosi la Mulungu pa mapewa awo pa mitengo yake yonyamulira monga momwe Mose analamulira molingana ndi mawu a Yehova.


Akerubiwo anatambalitsa mapiko awo pamwamba pa Bokosi la Chipangano ndipo anaphimba bokosilo pamodzi ndi mitengo yonyamulira.


Iye analikuta bokosilo ndi golide wabwino kwambiri mʼkati mwake ndi kunja komwe. Anapanganso mkombero wagolide kuzungulira bokosilo.


Kenaka anapanga mizati yamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide.


Ine ndinayankha kuti, “Mbuye wanga mukudziwa ndinu.” Tsono iye anandiwuza kuti, “Amenewa ndi amene anatuluka mʼmazunzo aakulu aja. Anachapa mikanjo yawo naziyeretsa mʼmagazi a Mwana Wankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa