Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tsika, chenjeza anthu, kuti angapyolere kwa Yehova kudzaona, ndipo angagwe ambiri a iwowa.
Eksodo 34:3 - Buku Lopatulika Palibe munthu akwere ndi iwe, asaonekenso munthu aliyense m'phiri monse; ndi zoweta zazing'ono kapena zoweta zazikulu zisadye kuphiri kuno. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Palibe munthu akwere ndi iwe, asaonekenso munthu aliyense m'phiri monse; ndi zoweta zazing'ono kapena zoweta zazikulu zisadye kuphiri kuno. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Usabwere ndi wina aliyense, ndipo wina asaoneke pa mbali iliyonse ya phirilo. Nkhosa kapena ng'ombe zisadzadye pa tsinde la phirilo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Palibe amene abwere nawe kapena kuoneka pena paliponse pafupi ndi phiri. Ndipo ngakhale nkhosa kapena ngʼombe zisadye mʼmbali mwa phirilo.” |
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tsika, chenjeza anthu, kuti angapyolere kwa Yehova kudzaona, ndipo angagwe ambiri a iwowa.
Ndipo musakhale munthu m'chihema chokomanako pakulowa iye kuchita chotetezera m'malo opatulika, kufikira atuluka, atachita chotetezera yekha, ndi mbumba yake, ndi msonkhano wonse wa Israele.
Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Khristu Yesu,
pakuti sanakhoze kulola cholamulidwacho. Ingakhale nyama ikakhudza phirilo, idzaponyedwa miyala;