Ndipo panali zitatha kumwa ngamira, munthuyo anatenga mphete yagolide ya kulemera kwake sekeli latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ake, kulemera kwake masekeli khumi a golide.
Eksodo 32:3 - Buku Lopatulika Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolide zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolide zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthuwo adavuladi nsapule zao, ndipo adabwera nazo kwa Aroni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero anthu onse anavula ndolo zagolide ndi kubwera nazo kwa Aaroni. |
Ndipo panali zitatha kumwa ngamira, munthuyo anatenga mphete yagolide ya kulemera kwake sekeli latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ake, kulemera kwake masekeli khumi a golide.
Ndipo anampatsa Yakobo milungu yachilendo yonse inali m'manja mwao, ndi mphete zinali m'makutu mwao: ndipo Yakobo anazibisa pansi pa mtengo wathundu unali pa Sekemu.
Ndipo Aroni ananena nao, Thyolani mphete zagolide zili m'makutu a akazi anu, a ana anu aamuna ndi aakazi, ndi kubwera nazo kwa ine.
Ndipo anazilandira ku manja ao, nachikonza ndi chozokotera, nachiyenga mwanawang'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.
Amene ataya golide, namtulutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golide; iye napanga nazo mulungu; iwo agwada pansi, inde alambira.
Abwera ndi siliva wa ku Tarisisi, wosulasula wopyapyala ndi golide wa ku Ufazi, ntchito ya mmisiri ndi manja a woyenga; zovala zao ndi nsalu ya madzi ndi yofiirira; zonsezi ndi ntchito za muomba.