Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 35:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo anampatsa Yakobo milungu yachilendo yonse inali m'manja mwao, ndi mphete zinali m'makutu mwao: ndipo Yakobo anazibisa pansi pa mtengo wathundu unali pa Sekemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anampatsa Yakobo milungu yachilendo yonse inali m'manja mwao, ndi mphete zinali m'makutu mwao: ndipo Yakobo anazibisa pansi pa mtengo wathundu unali pa Sekemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Motero milungu yonse yachilendo imene ana ake anali nayo, adaipereka kwa Yakobe, pamodzinso ndi ndolo zakukhutu zimene ankavala. Zonsezo adazifotsera patsinde pa mtengo wa thundu pafupi ndi Sekemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Choncho anamupatsa Yakobo milungu yachilendo yonse imene anali nayo pamodzi ndi ndolo. Iye anazikwirira pansi pa mtengo wa thundu ku Sekemu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 35:4
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anapitirira m'dzikomo kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m'dzikomo nthawi yomweyo.


tinyamuke, tikwere tinke ku Betele: ndipo tidzamanga kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anandivomereza tsiku la mavuto anga, ndiponso anali ndi ine m'njira m'mene ndinapitamo.


Ndipo anapita ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera mizinda yakuwazinga, ndipo sanalondole ana a Yakobo.


Ndipo anatenga mwanawang'ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israele.


Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze;


Ndipo mudzaipitsa chokuta cha mafano ako, osema asiliva, ndi chomata cha mafano ako osungunula agolide; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Chokani.


Ndipo ndidzamlanga chifukwa cha masiku a Abaala amene anawafukizira, navala mphete za m'mphuno, ndi zokometsera zake, natsata omkonda, nandiiwala Ine, ati Yehova.


Mafano osema a milungu yao muwatenthe ndi moto; musamasirira siliva ndi golide zili pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.


Koma muzichita nao motero: mukapasule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao, ndi kutentha mafano ao osema ndi moto.


Pamenepo anasonkhana eni ake onse a ku Sekemu, ndi nyumba yonse ya Milo, namuka namlonga Abimeleki ufumu pa thundu wa choimiritsa chili mu Sekemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa