Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 32:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kotero anthu onse anavula ndolo zagolide ndi kubwera nazo kwa Aaroni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolide zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolide zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Anthuwo adavuladi nsapule zao, ndipo adabwera nazo kwa Aroni.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 32:3
10 Mawu Ofanana  

Ngamira zija zitatha kumwa, mlendo uja anatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli ndi zibangiri zagolide ziwiri zolemera masekeli 100.


Choncho anamupatsa Yakobo milungu yachilendo yonse imene anali nayo pamodzi ndi ndolo. Iye anazikwirira pansi pa mtengo wa thundu ku Sekemu.


Aaroni anawayankha kuti, “Vulani ndolo zagolide zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi aakazi ndipo muzibweretse kwa ine.”


Choncho Aaroni analandira golideyo ndipo anamuwumba ndi chikombole ndi kupanga fano la mwana wangʼombe. Kenaka anthu aja anati, “Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.”


Kotero Aisraeli anavula zodzikometsera zawo pa phiri la Horebu.


ndolo ndi zibangiri, nsalu zophimba pa nkhope,


Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo ndipo amayeza siliva pa masikelo; amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu, kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.


Siliva wosula amabwera naye kuchokera ku Tarisisi ndipo golide amachokera naye ku Ufazi. Mafanowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi odziwa kuzokota golide. Tsono mafanowo amawaveka zovala za mtundu wamtambo ndi pepo. Yonseyo ndi ntchito ya anthu a luso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa