Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 32:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Choncho Aaroni analandira golideyo ndipo anamuwumba ndi chikombole ndi kupanga fano la mwana wangʼombe. Kenaka anthu aja anati, “Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo anazilandira ku manja ao, nachikonza ndi chozokotera, nachiyenga mwanawang'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anazilandira ku manja ao, nachikonza ndi chozokotera, nachiyenga mwanawang'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsono Aroni adalandira golideyo kumanja kwa anthuwo, ndipo adamsungunula, napanga fano la mwanawang'ombe m'chikombole. Ndipo anthu adayamba kufuula kuti, “Inu Aisraele, nayi milungu yanu imene idakutulutsani ku Ejipito.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 32:4
36 Mawu Ofanana  

Itapempha nzeru, mfumuyo inapanga mafano awiri a ana angʼombe. Mfumuyo inati kwa anthuwo, “Mwakhala mukupita ku Yerusalemu nthawi yayitali. Iwe Israeli, nayi milungu yako imene inakutulutsa mʼdziko la Igupto.”


Iye anakhazikitsa chikondwerero pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chitatu, lofanana ndi tsiku la chikondwerero cha ku Yuda, ndipo ankapereka nsembe pa guwa. Izi ankachita ku Beteli, kupereka nsembe kwa ana angʼombe amene anapanga. Ndipo ku Beteliko anayikako ansembe pa malo achipembedzo amene anamanga.


Yehu anati, “Itanitsani msonkhano wodzalemekeza Baala.” Ndipo analengeza za msonkhanowo.


Koma Yehuyo sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Israeli kupembedza mafano a golide a ana angʼombe ku Beteli ndi ku Dani.


Ndipo iye anasankha ansembe akeake a pa malo opatulika ndi a mafano a mbuzi ndi mwana wangʼombe amene anapanga.


“Ndipo tsopano inu mwakonzekera kutsutsana ndi ufumu wa Yehova, umene uli mʼmanja mwa zidzukulu za Davide. Inu ndithu mulipo ankhondo ambirimbiri ndipo muli ndi ana angʼombe agolide amene Yeroboamu anapanga kuti akhale milungu yanu.


Ngakhale pamene iwo anadziwumbira fano la mwana wangʼombe ndi kuti, ‘Uyu ndi mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto,’ kapena pamene anachita chipongwe choopsa.


“Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo.


Choncho musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide kuti muziyipembedza pamodzi ndi Ine.’ ”


“Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko.


Mayina a ana a Israeli uwazokote pa miyala iwiriyo, monga momwe amachitira mmisiri wozokota miyala. Ndipo uyike miyalayo mu zoyikamo zake zagolide.


“Utenge miyala iwiri ya onikisi ndipo uzokotepo mayina a ana a Israeli.


Anthu ataona kuti Mose akuchedwa kutsika mʼphiri, anasonkhana kwa Aaroni ndipo anati, “Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.”


Choncho ine ndinawawuza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi zokometsera zagolide azivule.’ Choncho iwo anandipatsa golide, ndipo ndinamuponya pa moto ndi kupanga fano la mwana wangʼombeyu.”


Kotero anthu onse anavula ndolo zagolide ndi kubwera nazo kwa Aaroni.


Ndipo Yehova anawakantha anthuwo ndi mliri chifukwa anawumiriza Aaroni kuti awapangire fano la mwana wangʼombe.


Aaroni ataona izi, anamanga guwa lansembe patsogolo pa mwana wangʼombeyo ndipo analengeza kuti, “Mawa kudzakhala chikondwerero cha Yehova.”


Pamenepo Yehova anati kwa Mose, “Tsika msanga, chifukwa anthu ako amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto aja adziyipitsa kwambiri.


Iwo apatuka mwamsanga kuleka kutsatira zimene ndinawalamula. Ndiye adzipangira fano la mwana wangʼombe. Aligwadira ndi kuliperekera nsembe nʼkumati, ‘Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ”


Pamenepo mudzawononga mafano anu okutidwa ndi siliva ndiponso zifanizo zanu zokutidwa ndi golide; mudzawataya ngati zinthu zonyansa ndipo mudzati, “Zichoke zonsezi!”


Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo ndipo amayeza siliva pa masikelo; amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu, kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.


Iye sanaleke za chiwerewere zimene anaziphunzira ku Igupto. Paja akanali mtsikana anyamata ankagona naye. Iwo ankamusisita mawere akanali anthete nachita naye zachiwerewere.


Anthu amene amakhala mu Samariya akuchita mantha chifukwa cha fano la mwana wangʼombe ku Beti-Aveni. Anthu ake adzalirira fanolo, chimodzimodzinso ansembe ake adamawo, amene anakondwera ndi kukongola kwake, chifukwa lachotsedwa pakati pawo ndi kupita ku ukapolo.


Tsopano akunka nachimwirachimwirabe; akudzipangira mafano pogwiritsa ntchito siliva wawo, zifanizo zopangidwa mwaluso, zonsezo zopangidwa ndi amisiri. Amanena za anthu awa kuti, “Amatenga munthu ndi kumupereka nsembe ndipo amapsompsona fano la mwana wangʼombe.”


“Tsono popeza ndife ana a Mulungu, tisaganize kuti umulungu wake ndi wofanana ndi ndalama zagolide, zasiliva, mwala, kapenanso fanizo lopangidwa mwaluso la nzeru za anthu.


Iyi ndi nthawi imene anapanga fano la mwana wangʼombe. Anapereka nsembe kwa fanoli nachita chikondwerero kulemekeza ntchito ya manja awo.


Musakhale anthu opembedza mafano, monga analili ena mwa iwo. Pakuti zalembedwa kuti, “Anthuwo anakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa. Kenaka anayimirira nayamba kuvina mwachilendo.”


Ine poyangʼana ndinaona kuti inu munachimwira Yehova Mulungu wanu. Munadzipangira fano lowumbidwa ngati mwana wangʼombe. Inuyo munapatuka msanga kuchoka pa njira imene Yehova anakulamulirani.


Gideoni anatinso, “Ine ndikupemphani chinthu chimodzi. Aliyense wa inu andipatse ndolo zomwe anafunkha ku nkhondo.” (Adani aja anali ndi ndolo zagolide popeza anali Aismaeli).


Gideoni anagwiritsa ntchito golide uja kupanga efodi, ndipo anakamuyika ku mzinda wake ku Ofura. Tsono Aisraeli onse anasiya kupembedza Yehova nayamba kupembedza efodiyo kumeneko. Ichi chinasanduka msampha kwa Gideoni ndi banja lake lonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa