Ndipo panali zitatha kumwa ngamira, munthuyo anatenga mphete yagolide ya kulemera kwake sekeli latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ake, kulemera kwake masekeli khumi a golide.
Eksodo 32:2 - Buku Lopatulika Ndipo Aroni ananena nao, Thyolani mphete zagolide zili m'makutu a akazi anu, a ana anu aamuna ndi aakazi, ndi kubwera nazo kwa ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aroni ananena nao, Thyolani mphete zagolide zili m'makutu a akazi anu, a ana anu aamuna ndi aakazi, ndi kubwera nazo kwa ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Aroni adauza anthuwo kuti, “Vulani nsapule zagolide kukhutu kwa akazi anu, kwa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi omwe, ndipo mubwere nazo kwa ine.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aaroni anawayankha kuti, “Vulani ndolo zagolide zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi aakazi ndipo muzibweretse kwa ine.” |
Ndipo panali zitatha kumwa ngamira, munthuyo anatenga mphete yagolide ya kulemera kwake sekeli latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ake, kulemera kwake masekeli khumi a golide.
Ndipo ndinamfunsa iye kuti, Ndiwe mwana wa yani kodi? Ndipo anati, Ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori amene anambalira iye Milika: ndipo ndinaika mphete pambuyo pake ndi zingwinjiri pa manja ake.
Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolide zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni
Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ake, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m'makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zigwinjiri, zonsezi zokometsera za golide; inde yense wakupereka kwa Yehova chopereka chagolide.
Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.
Ndipo mudzaipitsa chokuta cha mafano ako, osema asiliva, ndi chomata cha mafano ako osungunula agolide; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Chokani.
Unatenganso zokometsera zako zokoma za golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndinakupatsa, ndi kudzipangira mafano a amuna, ndi kuchita nao chigololo.
Pakuti sanadziwe kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumchulukitsira siliva ndi golide, zimene anapanga nazo Baala.