Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 35:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ake, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m'makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zigwinjiri, zonsezi zokometsera za golide; inde yense wakupereka kwa Yehova chopereka chagolide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ake, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m'makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zigwinjiri, zonsezi zokometsera za golide; inde yense wakupereka kwa Yehova chopereka chagolide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Kudabwera amuna ndi akazi omwe. Munthu aliyense malinga ndi kufuna kwake adabwera ndi zokometsera zomangira zovala, nsapule zakukhutu, mphete, ukufu wam'khosi, ndi zokometsera zina zagolide. Munthu aliyense adabwera ndi zagolide zimene adazipatula kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Onse amene anali ndi mtima wofuna, amuna ndi amayi omwe anabwera kudzapereka zodzikometsera zagolide za mtundu uliwonse: zomangira zovala, ndolo, mphete ndi zokometsera. Onse anapereka golide wawo monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 35:22
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Yowasi anati kwa ansembe, Landirani ndalama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo ndalama za otha msinkhu, ndalama za munthu aliyense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m'mtima mwake kuti abwere nazo kunyumba ya Yehova.


Pamenepo Hezekiya anayankha, nati, Tsopano mwadzipatulira kwa Yehova, senderani, bwerani nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika kunyumba ya Yehova. Ndi msonkhano unabwera nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika, ndi onse a mtima wofuna mwini anabwera nazo nsembe zopsereza.


Ndipo Aroni ananena nao, Thyolani mphete zagolide zili m'makutu a akazi anu, a ana anu aamuna ndi aakazi, ndi kubwera nazo kwa ine.


Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolide zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni


Ndipo anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito ya chihema chokomanako, ndi ku utumiki wake wonse, ndi ku zovala zopatulika.


Ndipo aliyense kwao kunapezeka lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi, ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo.


Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.


mbera, ndi makoza, ndi nsalu za pankhope;


Ulemerero wa Lebanoni udzafika kwa iwe; mtengo wamlombwa, mtengo wamkuyu ndi mtengo wanaphini pamodzi, kukometsera malo a Kachisi wanga; ndipo ndidzachititsa malo a mapazi anga ulemerero.


Zoonadi, zisumbu zidzandilindira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisisi kutenga ana ako aamuna kutali, golide wao ndi siliva wao pamodzi nao, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele, popeza Iye wakukometsa iwe.


Ndinakukometseranso ndi zokometsera, ndi kuika zigwinjiri m'manja mwako, ndi unyolo m'khosi mwako.


Ndipo tabwera nacho chopereka cha Yehova, yense chimene anachipeza, zokometsera zagolide, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kuchita chotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.


Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa