Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 27:12 - Buku Lopatulika

Ndipo m'kupingasa kwa bwaloli pa mbali ya kumadzulo mukhale nsalu zotchingira za mikono makumi asanu; nsichi zake zikhale khumi, ndi makamwa ao khumi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo m'kupingasa kwa bwaloli pa mbali ya kumadzulo mukhale nsalu zochingira za mikono makumi asanu; nsichi zake zikhale khumi, ndi makamwa ao khumi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Muufupi mwake mwa bwalolo cha mbali yakuzambwe, pakhale nsalu zochinga, kutalika kwake mamita 23, ndi nsanamira khumi ndi masinde khumi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Mbali yakumadzulo ya bwalolo ikhale yotalika mamita 23 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga, nsichi khumi ndi matsinde khumi.

Onani mutuwo



Eksodo 27:12
4 Mawu Ofanana  

Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri;


Momwemonso pa mbali ya ku kumpoto mu utali mwake pakhale nsalu zotchingira za mikono zana limodzi mu utali mwake; ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsichizo ndi mitanda yake zikhale zasiliva.


Ndipo m'kupingasa kwake kwa bwalo pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mukhale mikono makumi asanu.


ndi nsalu zotchinga za kubwalo, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, lokhala ku chihema, ndi ku guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zake za ku ntchito zake zonse.