Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri;
Eksodo 26:25 - Buku Lopatulika Ndipo pakhale matabwa asanu ndi atatu, ndi makamwa ao asiliva, ndiwo makamwa khumi mphambu asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakhale matabwa asanu ndi atatu, ndi makamwa ao asiliva, ndiwo makamwa khumi mphambu asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero padzakhala mafulemu asanu ndi atatu okhala ndi masinde ake 16 asiliva, aŵiri pansi pa fulemu lililonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho pakhale maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri akhale pansi pa feremu iliyonse. |
Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri;
Ndipo akhale ophatikizika pamodzi patsinde, nakhalenso ophatikizika pamodzi kumutu kwake ndi mphete imodzi; azitero onse awiri; azikhala angodya ziwiri.
Ndipo panali matabwa asanu ndi atatu. Ndi makamwa ao asiliva, makamwa khumi kudza asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi.
Ndipo matalente zana limodzi a siliva ndiwo a kuyengera makamwa a malo opatulika, ndi makamwa a nsalu yotchinga; makamwa zana limodzi matalente zana limodzi, talente limodzi kamwa limodzi.