Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 38:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo matalente zana limodzi a siliva ndiwo a kuyengera makamwa a malo opatulika, ndi makamwa a nsalu yotchinga; makamwa zana limodzi matalente zana limodzi, talente limodzi kamwa limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo matalente zana limodzi a siliva ndiwo a kuyengera makamwa a malo opatulika, ndi makamwa a nsalu yotchinga; makamwa zana limodzi matalente zana limodzi, talente limodzi kamwa limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Siliva wolemera makilogaramu 3,400 adamangira masinde 100 a malo opatulika ndi a nsalu zochingira. Tsinde lililonse linkalira siliva wolemera makilogaramu 34.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Anagwiritsa ntchito siliva wolemera makilogalamu 3,400 kupanga matsinde 100 a ku malo wopatulika ndi makatani, ndipo makilogalamu 34 kupanga tsinde limodzi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 38:27
6 Mawu Ofanana  

Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri;


makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina.


Ndipo pakhale matabwa asanu ndi atatu, ndi makamwa ao asiliva, ndiwo makamwa khumi mphambu asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina.


ndipo uitchinge pa mizati inai ya mitengo wakasiya, zokuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide, ndi makamwa anai asiliva.


Munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo awiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kunka kwa owerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi awiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu.


Ndipo anapanga zokowera za mizati nsanamira ndi nsichi ndi masekeli aja chikwi chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu asanu, nakuta mitu yake, nazigwirizanitsa pamodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa