Ndipo chotsalacho pansalu yophimbayo, hafu yake ya nsalu yotsalirayo, itchinge pambuyo pake pa chihemacho.
Eksodo 26:13 - Buku Lopatulika Ndi mkono wa pa mbali ino, ndi mkono wa pa mbali inzake, wakutsalira mu utali wake wa nsalu zophimbazo, itchinge pambali zake za chihemacho, mbali ino ndi mbali ina, kumphimba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi mkono wa pa mbali yino, ndi mkono wa pa mbali inzake, wakutsalira m'utali wake wa nsalu za hemalo, ichinge pambali zake za Kachisi, mbali yino ndi mbali ina, kumphimba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ndipo nsalu ya masentimita 46 yotsalira m'litali mwake pa mbali ziŵiri, izidzalendeŵera ndi kuphimba mbali ziŵirizo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nsalu yotsalira ya masentimita 46 mulitali mwake mʼmbali zonse ziwiri idzalendewere kuphimba mbali ziwirizo. |
Ndipo chotsalacho pansalu yophimbayo, hafu yake ya nsalu yotsalirayo, itchinge pambuyo pake pa chihemacho.
Ndipo uzipangira hema chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi chophimba za zikopa za akatumbu pamwamba pake.
Utali wake wa nsalu yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu zonse zikhale za muyeso umodzi.
Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo.