Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 26:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo uzipangira hema chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi chophimba za zikopa za akatumbu pamwamba pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo uzipangira hema chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi chophimba za zikopa za akatumbu pamwamba pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Lona lija ulipangire chophimbira chake chofiira cha chikopa cha nkhosa zamphongo. Pambuyo pake upangenso chophimbira chotsiriza cha zikopa zofeŵa chodzayala pamwamba pa zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Upange chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake upangireponso chophimbira china cha zikopa za akatumbu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 26:14
14 Mawu Ofanana  

Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa mkati mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.


ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;


Ndi mkono wa pa mbali ino, ndi mkono wa pa mbali inzake, wakutsalira mu utali wake wa nsalu zophimbazo, itchinge pambali zake za chihemacho, mbali ino ndi mbali ina, kumphimba.


Ndipo aliyense kwao kunapezeka lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi, ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo.


ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;


Ndipo anasokera hemalo chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu pamwamba pake.


ndi chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiirira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi nsalu yotchinga yotsekera;


Chifukwa Inu mwakhala linga la aumphawi, linga la osowa m'kuvutidwa kwake, pobisalira chimphepo, mthunzi wa pa dzuwa, pamene kuomba kwa akuopsa kufanana ndi chimphepo chakuomba tchemba.


Ndipo padzakhala chihema cha mthunzi, nthawi ya usana yopewera kutentha, pothawira ndi pousa mvula ndi mphepo.


Ndinakuvekanso ndi nsalu zopikapika, ndi kukuveka nsapato za chikopa cha katumbu; ndinakuzenenga nsalu yabafuta, ndi kukuphimba ndi nsalu yasilika.


Ndipo achimange ndi chipangizo zake zonse m'chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kuziika pa chonyamulira.


azinyamula nsalu zophimba za Kachisi, ndi chihema chokomanako, chophimba chake, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu chili pamwamba pake, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihema chokomanako;


akati amuke a m'chigono, Aroni ndi ana ake aamuna azilowa, natsitse nsalu yotchinga, ndi kuphimba nayo likasa la mboni,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa