Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.
Eksodo 24:9 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri anakwerako; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri anakwerako; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mose, Aroni, Nadabu ndi Abihu ndiponso anthu 70 mwa atsogoleri aja a Aisraele, adakwera phiri, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Mose pamodzi ndi Aaroni, Nadabu, Abihu ndi akuluakulu makumi asanu ndi awiri a Israeli aja anakwera ku phiri, |
Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.
Ndipo Yehova anati kwa iye, Muka, tsika; nukwere iwe ndi Aroni pamodzi ndi iwe; koma ansembe ndi anthu asapyole kukwera kwa Yehova, angawapasule.
Ndipo Iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali;
Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.
Ananenanso, Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona Ine ndi kukhala ndi moyo.
Chaka chimene mfumu Uziya anafa, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando wachifumu wautali, ndi wotukulidwa, ndi zovala zake zinadzala mu Kachisi.
Koma kunena za kalonga, iye akhale m'menemo monga kalonga kudya mkate pamaso pa Yehova; alowe kunjira ya kukhonde la chipata, natulukire njira yomweyi.
Ndipo ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu anatenga yense mbale yake ya zofukiza, naikamo moto, naikapo chofukiza, nabwera nao pamaso pa Yehova moto wachilendo, umene sanawauze.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akulu a Israele, amene uwadziwa kuti ndiwo akulu a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku chihema chokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.