Eksodo 24:10 - Buku Lopatulika10 ndipo anapenya Mulungu wa Israele; ndipo pansi pa mapazi ake panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiro, ndi ngati thupi la thambo loti mbee. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 ndipo anapenya Mulungu wa Israele; ndipo pansi pa mapazi ake panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiri, ndi ngati thupi la thambo loti mbee. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 ndipo adaonana ndi Mulungu wa Aisraele. Pansi pa mapazi ake panali china chooneka ngati mseu wopangidwa ndi mwala wa safiro woyalidwa bwino, wa maonekedwe onga thambo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 ndipo anaona Mulungu wa Israeli. Pansi pa mapazi ake panali njira yoyendamo yopangidwa ndi mwala wa safiro woyalidwa bwino wa maonekedwe owala ngati thambo. Onani mutuwo |