Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadye mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo.
Koma iwe, uime kuno ndi Ine, ndinene ndi iwe malamulo onse, ndi malemba, ndi maweruzo, amene uziwaphunzitsa, kuti awachite m'dziko limene ndiwapatsa likhale laolao.
Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova, monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku, osadya mkate osamwa madzi, chifukwa cha machimo anu onse mudachimwa, ndi kuchita choipacho pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.