Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 4:2 - Buku Lopatulika

2 kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai. Ndipo Iye sanadye kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai. Ndipo Iye sanadye kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana ankamuyesa. Yesu sankadya kanthu masiku amenewo, ndipo pamene masikuwo adatha, adamva njala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 kumene anayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anayi. Sanadye kena kalikonse pa masiku amenewo, ndipo pa mapeto pake anamva njala.

Onani mutuwo Koperani




Luka 4:2
16 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.


Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvu ya chakudya chimenecho masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika kuphiri la Mulungu ku Horebu.


Muka, sonkhanitsa Ayuda onse opezeka mu Susa, nimundisalire, osadya osamwa masiku atatu, usiku ndi usana, ine ndemwe ndi anamwali anga tidzasala momwemo, ndipo motero ndidzalowa kwa mfumu, ndiko kosalingana ndi lamulo; ndikaonongeka tsono ndionongeke.


Ndipo Mose analowa m'kati mwa mtambo, nakwera m'phirimo; ndipo Mose anakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku.


Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadye mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo.


Ndipo analalikira, nanena mu Ninive mwa lamulo la mfumu ndi nduna zake, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng'ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi;


Ndipo mamawa, m'mene Iye analinkunkanso kumzinda, anamva njala.


Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pake anamva njala.


Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mkate.


ndipo pamenepo panali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wake, motero anakhala pachitsime.


Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova, monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku, osadya mkate osamwa madzi, chifukwa cha machimo anu onse mudachimwa, ndi kuchita choipacho pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.


Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova masiku makumi anai usana ndi usiku ndinagwa pansiwa; popeza Yehova adati kuti adzakuonongani.


Muja ndinakwera m'phiri kukalandira magome amiyala, ndiwo magome a chipangano chimene Yehova anapangana ndi inu, ndinakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku; osadya mkate osamwa madzi.


Pakuti popeza adamva zowawa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.


Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.


Ndipo Mfilistiyo anayandikira m'mawa ndi madzulo, nadzionetsera masiku makumi anai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa