Eksodo 23:4 - Buku Lopatulika Ukakomana ndi ng'ombe kapena bulu wa mdani wako zilinkusokera, uzimbwezera izo ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ukakomana ndi ng'ombe kapena bulu wa mdani wako zilimkusokera, uzimbwezera izo ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ukaona ng'ombe ya mdani wako ikusokera, kapena bulu wake, utenge ukampatse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ngati ukumana ndi ngʼombe kapena bulu wa mdani wako zitasochera, uwonetsetse kuti wazitenga kupita nazo kwa mwini wakeyo. |
kapena anapeza chinthu chotayika, nanenapo bodza, nalumbira pabodza; pa chimodzi cha izi zonse amachita munthu, ndi kuchimwapo;
Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.