Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 22:20 - Buku Lopatulika

Wakuphera nsembe mulungu wina, wosati Yehova yekha, aonongeke konse.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Wakuphera nsembe mulungu wina, wosati Yehova yekha, aonongeke konse.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Aliyense wopereka nsembe kwa milungu, osati kwa Chauta yekha, aphedwe ameneyo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Aliyense wopereka nsembe kwa mulungu wina osati Yehova awonongedwe.

Onani mutuwo



Eksodo 22:20
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya anati kwa iwo, Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense. Nawagwira, ndipo Eliya anapita nao ku mtsinje wa Kisoni, nawapha pamenepo.


Ndipo kunali, atatsiriza kupereka nsembe yopsereza, Yehu anati kwa otumikira ndi atsogoleri, Lowani, akantheni; asatuluke ndi mmodzi yense. Nawakantha ndi lupanga lakuthwa; ndi otumikira ndi atsogoleri anawataya kubwalo, namuka kumzinda wa nyumba ya Baala.


ndi kuti yense wosafuna Yehova Mulungu wa Israele aphedwe, ngakhale wamng'ono kapena wamkulu, wamwamuna kapena wamkazi.


Usampsinja mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m'dziko la Ejipito.


wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwanawang'ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.


ungachite pangano ndi iwo okhala m'dzikomo; ndipo angachite chigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zake;


ndipo ndinanena nao, Aliyense ataye zonyansa za pamaso pake, nimusadzidetsa ndi mafano a Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Ndipo asamapheranso milungu ina nsembe zao, zimene azitsata ndi chigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.


Ndipo mlendo akagonera m'dziko mwanu, musamamsautsa.


Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.


Ndipo Yehova anamvera mau a Israele, napereka Akanani; ndipo anawaononga konse ndi mizinda yao yomwe; natcha dzina lake la malowo Horoma.


Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa chakudya ndi chovala.


Koma mneneri wakuchita modzikuza ndi kunena mau m'dzina langa, amene sindinamlamulire anene, kapena kunena m'dzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe.


Ana obadwa nao a mbadwo wachitatu alowe m'msonkhano wa Yehova.


Musamaipsa mlandu wa mlendo, kapena wa ana amasiye; kapena kutenga chikole chovala cha mkazi wamasiye;