Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso.
Eksodo 21:36 - Buku Lopatulika Kapena kudadziwika kuti ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kapena kudadziwika kuti ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma kukadziŵika kuti ng'ombeyo inkangogunda anthu, mwiniwake osaimanga, mwiniwakeyo ayenera kulipira pakupereka ng'ombe yamoyo chifukwa cha yakufayo. Tsono ng'ombe yakufayo ikhale yake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma zikadziwika kuti ngʼombeyo inali ndi khalidwe logunda, ndipo mwini wake samayitsekera mʼkhola, mwini ngʼombeyo alipire ngʼombe ina yamoyo koma atenge yakufayo.” |
Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso.
Ng'ombe ya mwini ikapweteka ng'ombe ya mnzake, nifa, azigulitsa ng'ombe yamoyoyo, nagawe ndalama zake; naigawe, ndi yakufa yomweyo.
Munthu akaba ng'ombe, kapena nkhosa, nakaipha kapena kuigulitsa, azilipa ng'ombe zisanu pa ng'ombeyo, ndi nkhosa zinai pa nkhosayo.