Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 21:29 - Buku Lopatulika

29 Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Koma ngati khalidwe lake la ng'ombeyo linali kumangogunda anthu, ndipo mwiniwake adachenjezedwa, koma iye osaimanga, ng'ombeyo ikapha munthu wamwamuna kapena wamkazi, iponyedwe miyala ndithu. Ndipo mwiniwakeyonso aphedwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Koma ngati ngʼombeyo inali ndi chizolowezi chogunda anthu ndipo mwini wakeyo anachenjezedwa koma iye sanayimange ndipo yapha mwamuna kapena mkazi, ngʼombeyo iponyedwe miyala ndipo mwini wakeyo aphedwenso.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 21:29
5 Mawu Ofanana  

Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; padzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi padzanja la munthu, padzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu.


Ng'ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng'ombeyo, osadya nyama yake; koma mwini ng'ombeyo azimasuka.


Akamuikira dipo, azipereka chiombolo cha moyo wake monga mwa zonse adamuikira.


Kapena kudadziwika kuti ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa