Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 21:28 - Buku Lopatulika

28 Ng'ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng'ombeyo, osadya nyama yake; koma mwini ng'ombeyo azimasuka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Ng'ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng'ombeyo, osadya nyama yake; koma mwini ng'ombeyo azimasuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 “Ng'ombe ikapha munthu wamwamuna kapena wamkazi ndi nyanga, iponyedwe miyala, ndipo nyama yake musadye. Koma mwiniwake wa ng'ombeyo asalangidwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 “Ngati ngʼombe ipha munthu wamwamuna kapena wamkazi ndi nyanga yake, iponyedwe miyala ndipo nyama yake isadyedwe. Ndipo mwini ngʼombeyo asayimbidwe mlandu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 21:28
5 Mawu Ofanana  

Ndipo akagulula dzino la mnyamata wake, kapena dzino la mdzakazi wake, azimlola amuke waufulu chifukwa cha dzino lake.


Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso.


Ng'ombeyo ikatunga mnyamata kapena mdzakazi, azipatsa mbuye wake ndalama za masekeli a siliva makumi atatu, ndipo ng'ombeyo aiponye miyala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa