Ndipo panali pamene Yakobo anaona Rakele, mwana wamkazi wa Labani, mlongo wake wa amake, ndi nkhosa za Labani mlongo wake wa amake, Yakobo anayandikira nagubuduza kuuchotsa mwala pachitsime, nazimwetsa zoweta za Labani, mlongo wake wa amake.
Eksodo 2:19 - Buku Lopatulika Ndipo anati iwo, Munthu Mwejipito anatilanditsa m'manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati iwo, Munthu Mwejipito anatilanditsa m'manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo aja adayankha kuti, “Mwejipito wina ndiye amene watitchinjiriza kwa abusa, ndipo watitungira madzi omwetsa zoŵeta zonsezi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atsikanawo anayankha kuti, “Mwigupto wina ndiye watilanditsa kwa abusa. Ndiponso anatitungira madzi ndi kumwetsa ziweto zathu.” |
Ndipo panali pamene Yakobo anaona Rakele, mwana wamkazi wa Labani, mlongo wake wa amake, ndi nkhosa za Labani mlongo wake wa amake, Yakobo anayandikira nagubuduza kuuchotsa mwala pachitsime, nazimwetsa zoweta za Labani, mlongo wake wa amake.
Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo, Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro aakulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani.
Ndipo anati kwa ana ake aakazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye chakudya.